Psalms 35:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene amakondwera poona kuti ndili pa mavuto, muŵachititse manyazi, muŵasokoneze kwathunthu. Amene amayesa kuti akupambana ine, achite manyazi ndipo anyozeke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene amakondwera ndi masautso anga achite manyazi ndi kusokonezeka. Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana, avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Acite manyazi, nadodome iwo akukondwera cifukwa ca coipa cidandigwera: Abvekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.