Psalms 35:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma amene amafunitsitsa kuti ndipezeke wosalakwa, afuule ndi chimwemwe ndipo asangalale. Anene nthaŵi zonse kuti, “Chauta ndi wamkulu. Amakondwera akaona mtumiki wake zamuyendera bwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa, afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo. Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke, Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Apfuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera naco cilungamo canga: Ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, Amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wace.