Psalms 36:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uchimo umalankhula mu mtima wa munthu wosamvera Mulungu. Alibe mantha ndi Mulungu m'maganizo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. Uthenga uli mu mtima mwanga wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa: Mu mtima mwake mulibe kuopa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Colakwa ca woipayo cimati m'kati mwa mtima wanga, Palibe kuopa Mulungu pamaso pace.