Psalms 36:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu, chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu. Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu; Maweruzo anu akunga cozama cacikuru: Yehova, musunga munthu ndi nyama.