Psalms 37:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba koma sindinaonepo olungama akusiyidwa kapena ana awo akupempha chakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinali mwana ndipo ndakalamba: Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, Kapena mbumba zace zirinkupempha cakudya.