Psalms 37:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye: Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace, Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.