Psalms 39:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidati, “Ndidzasamala zochita zanga, kuti ndisachimwe polankhula. Ndidzatseka pakamwa panga nthaŵi zonse pamene anthu oipa ali nane.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo, kwa Yedutuni. Salimo la Davide. Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide. Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe; ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, Kuti ndingacimwe ndi lilime langa: Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam'kamwa, Pokhala woipa ali pamaso panga.