Psalms 39:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumalanga munthu pakumdzudzula chifukwa cha uchimo wake. Mumaonongeratu zimene iye amazikonda, monga m'mene chimachitira chifukufuku. Zoonadi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo; mumawononga chuma chawo monga njenjete; munthu aliyense ali ngati mpweya. Sela
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula cifukwa ca mphulupulu, Mukanganula kukongola kwace monga mumacita ndi kadzoce: Indedi, munthu ali yense ali cabe.