Psalms 39:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mverani pemphero langa, Inu Chauta, mumve kulira kwanga. Musakhale chete pamene ndikulirira Inu. Ndine mlendo wanu wosakhalitsa, munthu wongokhala nawo monga adaachitira makolo anga onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Imvani pemphero langa Inu Yehova, mverani kulira kwanga kopempha thandizo; musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu, popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa; monga anachitira makolo anga onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo cherani khutu kulira kwanga; Musakhale cete pa misozi yanga: Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, Wosakhazikika, monga makolo anga onse.