Psalms 39:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi, amangovutika ndi zachabechabe. Munthu amakundika chuma, koma amene adzachidye ndi wosadziŵika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku: Iye amangovutika koma popanda phindu; amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indedi munthu ayenda ngati mthunzi: Indedi abvutika cabe: Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?