Psalms 40:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; Ndipo anandilola, namva kupfuula kwanga.