Psalms 40:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu: Iwo akukonda cipulumutso canu asaleke kunena, Abuke Yehova.