Psalms 40:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga, nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga. Ambiri adzaona, nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapatsa Nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, cilemekezo ca kwa Mulungu wanga; Ambiri adzaciona, nadzaopa, Ndipo adzakhulupirira Yehova.