Psalms 40:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazicita nzambiri, Ndipo zolingirira zanu za pa ife; Palibe wina wozifotokozera Inu; Ndikazisimba ndi kuzichula, Zindicurukira kuziwerenga.