Psalms 40:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simudafune nsembe ndi zopereka, koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera. Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapempha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna, koma makutu anga mwawatsekula; zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo Inu simunazipemphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nsembe ndi copereka simukondwera nazo; Mwanditsegula makutu: Nsembe yopsereza ndi yamacimo simunapempha.