Psalms 41:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wodala iye amene asamalira wosauka: Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa: