Psalms 41:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi; Ndipo musampereke ku cifuniro ca adani ace.