Psalms 42:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zinthu izi ndimazikumbukira pamene ndikukhuthula moyo wanga: momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu, kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko pakati pa anthu a pa chikondwerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndizikumbukila izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, Pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu, Ndinawatsogolera ku nyumba ya Mulungu, ndi mau akuyimbitsa ndi kuyamika, Ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.