Psalms 42:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimafunsa Mulungu, thanthwe langa, kuti, “Mwandiiŵaliranji? Ndiziyenderanji ndilikulira chifukwa chondipsinja mdani wanga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa, “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala cifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira Cifukwa ca kundipsinja mdaniyo?