Psalms 44:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu, ife tidamva ndi makutu athu, makolo athu adatiwuza za ntchito zimene mudagwira pa masiku ao, masiku amakedzana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, Za nchitoyo mudaicita masiku ao, masiku akale.