Psalms 44:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mudapirikitsa mitundu ina ya anthu, koma makolo athu mudaŵakhazika m'dziko lao. Inu mudasautsa mitundu ina ya anthu, koma makolo athuwo Inu mudaŵapatsa ufulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena ndi kudzala makolo athu; Inu munakantha mitundu ya anthu, koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu munapitikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; Munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa,