Psalms 44:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo sadalande dziko ndi lupanga lao, sadapambane pa nkhondo ndi mphamvu zao. Koma adagonjetsa ndi mphamvu zanu, chifukwa cha kuŵala kwa nkhope yanu, pakuti mudakondwera nawodi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sanalanda dziko ndi lupanga lao, Ndipo mkono wao sunawapulumutsa: Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,