Psalms 45:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma. Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi. Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri wodziŵa kulemba bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Syosyanimu. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Nyimbo ya chikondi. Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati. Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu; lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima wanga usefukira naco cinthu cokoma: Ndinena zopeka ine za mfumu: Lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.