Psalms 45:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu ndinu wokongola kwambiri kuposa anzanu ena onse. Pakamwa panu pamatulutsa zokoma zokhazokha. Nchifukwa chake Mulungu wakudalitsani mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika, popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu ndinu wokongola ndithu kuposa ana a anthu; Anakutsanulirani cisomo pa milomo yanu: Cifukwa cace Mulungu anakudalitsani kosatha.