Psalms 45:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pitani ndi ulemerero wanuwo, kuti mukagonjetse adani anu onse, mukateteze zimene zili zoona, zachifatso ndi zachilungamo. Dzanja lanu lamanja likaonetse ntchito zanu zoopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pindulani, m'ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo; dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pindulani, m'ukulu wanu yendani, Kaamba ka coonadi ndi cifatso ndi cilungamo: Ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.