Psalms 45:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumakonda chilungamo ndipo mumadana ndi zoipa. Nchifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, wakusankhani. Wakudzozani ndi kukusangalatsani kupambana anzanu ena onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukonda cilungamo, ndipo mudana naco coipa: Cifukwa cace Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu Ndi mafuta a cikondwerero kuposa anzanu.