Psalms 45:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zovala zanu nzonunkhira mure, aloe ndi kasiya. Nyumba zanu zachifumu nzomangidwa ndi mnyanga. M'menemo zoimbira zansambo zimakusangalatsani,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya; kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zobvala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasya; M'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njobvu mwatoruka zoyimba za zingwe zokukondweretsani.