Psalms 47:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri a anthu a mitundu ina yonse amasonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu onse a pansi pano ndi ake a Mulungu, Iyeyo ndiye wamkulu kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akulu a anthu asonkhana Akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu: Pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; Akwezeka kwakukuru Iyeyo.