Psalms 49:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi, aliyense atha kuwona kuti ngakhale anthu anzeru amafa. Chimodzimodzi, anthu opusa ndi opulukira ayenera kufa ndi kusiyira ena chuma chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti aona anzeru amafa, Monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, Nasiyira ena cuma cao.