Psalms 49:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa, ndipo imfa idzakhala mbusa wao. Anthu olungama adzaŵapambana. Adzatsika kulunjika ku manda, matupi ao adzaola, kwao kudzakhala kumanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aikidwa m'manda ngati nkhosa; Mbusa wao ndi imfa: Ndipo m'mawa mwace oongoka mtima adzakhala mafumu ao; Ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pace padzasowa.