Psalms 49:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zakuya, ndipo ndidzalankhula zanzeru.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakamwa panga padzanena zanzeru; ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakamwa panga padzanena zanzeru; Ndipo cilingiriro ca mtima wanga cidzakhala ca cidziwitso.