Psalms 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, Apfuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; Nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.