Psalms 5:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani kulira kwanga, Inu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti ndikupempha chithandizo kwa Inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamvetsani mau a kupfuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga: Pakuti kwa Inu ndimapemphera,