Psalms 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndidzatha kuloŵa m'Nyumba mwanu chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu. Ndidzaŵeramitsa mutu pansi, kupembedza Inu m'Nyumba yanu yoyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu, ndidzalowa mʼNyumba yanu; mwa ulemu ndidzaweramira pansi kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, mwa kucuruka kwa cifundo canu ndidzalowa m'nyumba yanu: Ndidzagwada kuyang'ana Kacisi wanu woyera ndi kuopa Inu.