Psalms 5:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adani anga amalankhula mabodza okhaokha. Mtima wao umangofuna kuwononga. Mummero mwao muli ngati manda apululu, ndipo lilime lao limalankhula zonyenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike; mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko. Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; M'kati mwao m'mosakaza; M'mero mwao ndi manda apululu: Lilime lao asyasyalika nalo.