Psalms 50:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe wachita zinthu zimenezi, ndipo Ine ndakhala ndili chete. Unalikuganiza kuti ndimafanafana nawe. Koma tsopano ndikukudzudzula ndi kukuwonetsa zimene wachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete; umaganiza kuti ndine wofanana nawe koma ndidzakudzudzula ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi unazicita iwe, ndipo ndinakhala cete Ine; Unayesa kuti ndifanana nawe: Ndidzakudzudzula, ndi kucilongosola pamaso pako.