Psalms 51:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide; m'mene anamdzera Natani mneneriyo atalowa iye kwa Bateseba. Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundicitire ine cifundo, Mulungu, Monga mwa kukoma mtima kwanu; Monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu Mufafanize macimo anga.