Psalms 51:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndachimwira Inu, Inu nokha, ndachita choipa pamaso panu. Motero mwakhoza ponditchula wolakwa, simudalakwe pogamula mlandu wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa ndipo ndachita zoyipa pamaso panu, Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa Inu, Inu nokha, ndinacimwa, Ndipo ndinacicita coipaco pamaso panu: Kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, Mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.