Psalms 53:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Mahalati. Chilangizo cha Davide. Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citsiru cimati mumtima mwace, Kulibe Mulungu. Acita zobvunda, acita cosalungama conyansa; Kulibe wakucita bwino.