Psalms 53:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere? Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya, ndipo samutama Mulungu mopemba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi ochita zopanda pake sadziwa? Pomadya anthu anga monga akudya mkate; ndipo saitana Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi; anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi, ndipo sapemphera kwa Mulungu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi ocita zopanda pace sadziwa? Pomadya anthu anga monga akudya mkate; Ndipo saitana Mulungu.