Psalms 53:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, mantha ake amene sadaoneke ndi kale lonse. Pakuti Mulungu adzaononga adani okuzingani. Inu mudzaŵachititsa manyazi chifukwa Mulungu waŵakana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaopa kwakukuru, popanda cifukwa ca kuopa: Pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; Unawacititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.