Psalms 53:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni! Mulungu akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha, chipulumutso cha Israele chichokere m'Ziyoni! Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m'ndende, Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni! Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake, lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha, cipulumutso ca Israyeli cicokere m'Ziyoni! Pakubweretsa Mulungu anthu ace a m'ndende, Yakobo adzakondwera, Israyeli adzasekera.