Psalms 54:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu, pulumutseni ndi dzina lanu, onetsani ndi mphamvu zanu kuti ndine wosalakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Chilangizo cha Davide. Muja Azifi anamuka nauza Saulo, kuti, Kodi Davide sabisala kwathu nanga? Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu, ndipo mundiweruze ndi mphamvu yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.” Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu, Ndipo mundiweruze ndi mphamvuyanu.