Psalms 55:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu, amene akukhala pa mpando waufumu kuyambira kalekale, adzandimenyera nkhondo, adzaŵatsitsa adani anga chifukwa safuna kusintha khalidwe lao loipa, ndipo saopa Iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu adzamva, nadzawasautsa, ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, ndipo saopa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya, adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga, chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa ndipo saopa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu adzamva, nadzawasautsa, Ndiye wokhalabe ciyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, Ndipo saopa Mulungu.