Psalms 55:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau ake anali osalala kupambana batala, komabe mumtima mwake munali zankhondo. Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta, komabe anali ndi malupanga osololasolola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu ake ndi osalala kuposa batala komabe nkhondo ili mu mtima mwake; mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta, komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakamwa pace mposalala ngati mafuta amkaka, Koma mumtima mwace munali nkhondo: Mau ace ngofewa ngati mafuta oyenga, Koma anali malupanga osololasolola.