Psalms 55:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga m'dzenje lozama lachiwonongeko. Anthu okhetsa magazi ndi onyenga sadzafika ngakhale theka la masiku ao. Koma ine ndidzadalira Inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa kulowa mʼdzenje lachiwonongeko; anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo sadzakhala moyo theka la masiku awo, koma ine ndimadalira Inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira ku dzenje la cionongeko: Anthu okhetsa mwazi ndi acinyengo masiku ao sadzafikira nusu; Koma ine ndidzakhulupirira Inu.