Psalms 55:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuda nkhaŵa chifukwa adani anga akundifuulira, anthu oipa akundipsinja. Akundivutitsa kwambiri, akundikwiyira kosalekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa cha mawu a adani anga, chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa; pakuti andidzetsera masautso ndipo akundizunza mu mkwiyo wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca mau a mdani, Cifukwa ca kundipsinja woipa; Pakuti andisenza zopanda pace, Ndipo adana nane mumkwiyo.