Psalms 56:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti anthu akundizunza. Adani akundithira nkhondo ndi kundipsinja tsiku lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yonat-Elem-Rekokimu. Mikitamu wa Davide, muja Afilisti anamgwira m'Gati. Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati. Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri; tsiku lonse akundithira nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundicitire cifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza: Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.