Psalms 56:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda, mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha. Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace: Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; Anthu adzandicitanji?