Psalms 56:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mwaona kupiripita kwanga, mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga. Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulembe za kulira kwanga, mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu. Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muwerenga kuthawathawa kwanga: Sungani misozi yanga m'nsupa yanu; Kodi siikhala m'buku mwanu?